1 Kings 14:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele onse adzalira maliro ake, ndipo adzamuika, pakuti iye yekhayo mwa anthu a m'banja la Yerobowamu ndiye adzaikidwe ku manda, chifukwa Chauta, Mulungu wa Aisraele, wakondwa ndi iye yekha pa banja lonse la Yerobowamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aisraele onse adzamlira, nadzamuika, popeza iye yekha wa ana a Yerobowamu adzalowa m'manda; pakuti mwa iye mwapezedwa chokoma cha kwa Yehova Mulungu wa Israele m'nyumba ya Yerobowamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli onse adzalira maliro ake ndi kumuyika mʼmanda. Ndi yekhayo wa banja la Yeroboamu amene adzayikidwe mʼmanda, pakuti ndi mwa iye yekha mmene Yehova Mulungu wa Israeli wapezamo kanthu kabwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aisrayeli onse adzamlira, nadzamuika, popeza iye yekha wa ana a Yerobiamu adzalowa m'manda; pakuti mwa iye mwapezedwa cokoma ca kwa Yehova Mulungu wa Israyeli m'nyumba ya Yerobiamu.