1 Kings 14:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzagwedeza Israele ngati bango lapamadzi, ndipo adzachotsa anthu a ku Israele m'dziko labwinoli, limene Iye adapatsa makolo ao. Adzaŵamwazira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, chifukwa choti iwo adadzipangira mafano a Asera, mulungu wachikazi, nakwiyitsa Chauta pakutero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza Yehova adzawakantha Aisraele monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisraele m'dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Yufurate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova adzakantha Israeli, kotero kuti adzakhala ngati bango logwedera pa madzi. Iye adzazula Israeli mʼdziko labwino limene analipereka kwa makolo ake ndi kuwamwazira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, chifukwa anakwiyitsa Yehova pamene anapanga mafano a Asera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza Yehova adzawakantha Aisrayeli monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisrayeli m'dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Firate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova.