1 Kings 14:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mkazi wa Yerobowamu adachoka napita ku Tiriza. Atangofika pa khomo la nyumba yake, mwana uja adamwalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi wa Yerobowamu ananyamuka nachoka, nafika ku Tiriza; ndipo polowa iye pa khomo la nyumba yake anatsirizika mwanayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mkazi wa Yeroboamu anayimirira nachoka kupita ku Tiriza. Atangoponda pa khonde la nyumba yake, mwana uja anamwalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi wa Yerobiamu ananyamuka nacoka, nafika ku Tiriza; ndipo polowa iye pa khomo la nyumba yace anatsirizika mwanayo.