1 Kings 14:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito zonse za Yerobowamu, m'mene ankamenyera nkhondo ndi m'mene ankalamulira, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo machitidwe ena a Yerobowamu m'mene umo anachitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchito zina pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu, nkhondo zake ndi mmene ankalamulirira zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo macitidwe ena a Yerobiamu m'mene umo anacitira nkhondo, ndi m'mene umo anacitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.