1 Kings 14:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye Yerobowamu adauza mkazi wake kuti, “Tiye udzizimbaitse, munthu asakudziŵe kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu, ndipo upite ku Silo kwa mneneri Ahiya, amene adanena za ine, kuti ndidzakhala mfumu yolamulira anthu aŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yerobowamu ananena ndi mkazi wake, Unyamuke, nudzizimbaitse, ungadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu, nupite ku Silo; taona, kumeneko kuli Ahiya mneneri uja anandiuza ine ndidzakhala mfumu ya anthu awa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo Yeroboamu anati kwa mkazi wake, “Nyamuka ndipo udzibise kuti usadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yeroboamu, ndipo upite ku Silo. Kumeneko kuli mneneri Ahiya amene anandiwuza kuti ndidzakhala mfumu ya anthu awa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yerobiamu ananena ndi mkazi wace, Unyamuke, nudzizimbaitse, ungadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yerobiamu, nupite ku Silo; taona, kumeneko kuli Ahiya mneneri uja anandiuza ine ndidzakhala mfumu ya anthu awa.