1 Kings 14:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Rehobowamu, mwana wa Solomoni, anali mfumu ya ku Yuda. Anali wa zaka 41 nthaŵi imene ankaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Chauta adaausankha pakati pa mafuko onse a Aisraele, kuti anthu azimpembedzerako. Mai wake anali Naama, wa kwa Aamoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, m'mudzi m'mene Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele kukhazikamo dzina lake. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya ku Yuda. Iye analowa ufumu ali ndi zaka 41, ndipo analamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anawusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti ayikemo Dzina lake. Amayi ake anali Naama, wa ku Amoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rehabiamu mwana wa Solomo anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehabiamu anali wa zaka makumi anai mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, m'mudzi m'mene Yehova adausankha m'mafuko onse a Israyeli kukhazikamo dzina lace. Ndipo dzina la amace linali Naama M-amoni.