1 Kings 14:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo anthu a ku Yuda ankachita zoipa, ankachimwira Chauta kupambana m'mene adaachitira makolo ao onse, nakwiyitsa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ayuda anachita zoipa pamaso pa Yehova, namchititsa nsanje ndi zoipa zao anazichitazo, zakuposa zija adazichita makolo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Yuda anachita zoyipa pamaso pa Yehova kupambana mmene anachitira makolo awo ndipo Yehova anawakwiyira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ayuda anacita zoipa pamaso pa Yehova, namcititsa nsanje ndi zoipa zao anazicitazo, zakuposa zija adazicita makolo ao,