1 Kings 14:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalanda chuma cha ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi chuma cha ku nyumba ya mfumu. Adatenga zonse, ngakhalenso zishango zomwe zagolide zimene Solomoni adaapanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; inde anachotsa chonsecho, nachotsanso zikopa zagolide zonse adazipanga Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ananyamula chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso chuma cha ku nyumba ya mfumu. Anatenga chilichonse, ngakhalenso zishango zonse zagolide zimene Solomoni anapanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nacotsa cuma ca m'nyumba ya Yehova, ndi cuma ca m'nyumba ya mfumu; inde anacotsa conseco, nacotsanso zikopa zagolidi zonse adazipanga Solomo.