1 Kings 14:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono nthaŵi zonse mfumu ikamaloŵa m'Nyumba ya Chauta, alondawo ankatenga zishangozo, kenaka nkumazibwezera ku chipinda cha alonda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika, pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, olindirira aja anazinyamula, nabweranso nazo ku chipinda cha olindirirawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi zonse mfumu ikamapita ku Nyumba ya Yehova, alonda ankanyamula zishangozo, kenaka ankazisunga mʼchipinda cha alonda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika, pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, olindirira aja anazinyamula, nabweranso nazo ku cipinda ca olindirirawo.