1 Kings 14:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Rehobowamu adamwalira, naikidwa mu mzinda wa Davide m'manda momwe adaikidwa makolo ake. Mai wake uja anali Naama, wa mtundu wa Aamoni. Ndipo Abiya, mwana wa Rehobowamu, adaloŵa ufumu m'malo mwa bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mudzi wa Davide. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni, nalowa ufumu m'malo mwake Abiya mwana wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Rehobowamu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Amayi ake anali Naama wa ku Amoni. Ndipo Abiya analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nagona Rehabiamu ndi makolo ace, naikidwa kwa makolo ace m'mudzi wa Davide. Ndipo dzina la amace linali Naama M-amoni, nalowa ufumu m'malo mwace Abiya mwana wace.