1 Kings 14:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi wa Yerobowamu adadzizimbaitsadi, ndipo adapita ku Silo, nakafika ku nyumba ya Ahiya. Ahiya sankatha kupenya bwino, ankangoona ngati nkhungu, chifukwa cha ukalamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natero mkazi wa Yerobowamu, nanyamuka namka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanatha kupenya, popeza maso ake anali tong'o, chifukwa cha ukalamba wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mkazi wa Yeroboamu anadzibisa ndipo anapita ku nyumba ya Ahiya ku Silo. Tsono Ahiya sankatha kupenya bwino. Ankangoona kuti mbuu chifukwa cha ukalamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natero mkazi wa Yerobiamu, nanyamuka namka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanatha kupenya, popeza maso ace anali tong'o, cifukwa ca ukalamba wace.