1 Kings 14:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauza Ahiya kuti, “Taona, mkazi wa Yerobowamu akubwera kudzafunsa iwe za mwana wake, pakuti akudwala. Ndiye iwe udzamuuze zakutizakuti mkaziyo. Akafika adzadzibisa, nkukhala ngati mkazi wina.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananena ndi Ahiya, Taona, mkazi wa Yerobowamu akudza kukufunsa za mwana wake, popeza adwala; udzanena naye mwakutimwakuti; popeza kudzakhala pakulowa iye adzadzizimbaitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova nʼkuti atamuwuza Ahiya kuti, “Taona, mkazi wa Yeroboamu akubwera kudzafunsa iwe za mwana wake pakuti akudwala, ndiye udzamuyankhe zakutizakuti mkaziyo. Iye akafika, adzadzibisa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananena ndi Ahiya, Taona, mkazi wa Yerobiamu akudza kukufunsa za mwana wace, popeza adwala; udzanena naye mwakuti mwakuti; popeza kudzakhala pakulowa iye adzadzizimbaitsa.