1 Kings 14:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahiya atangomva mgugu wa mapazi ake akuloŵa pa khomo, adati “Loŵa, iwe mkazi wa Yerobowamu, bwanji ukudzibisa? Ndakutengera mau oŵaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika, pamene Ahiya anamva mgugu wa mapazi ake alinkulowa pakhomo, anati, Lowa mkazi iwe wa Yerobowamu, wadzizimbaitsiranji? Pakuti ine ndatumidwa kwa iwe ndi mau olasa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Ahiya atamva mgugu wa mapazi ake pa khomo, anati, “Lowa, iwe mkazi wa Yeroboamu. Bwanji ukudzibisa? Ine ndatumidwa kuti ndikuwuze nkhani yoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika, pamene Ahiya anamva mgugu wa mapazi ace alinkulowa pakhomo, anati, Lowa mkazi iwe wa Yerobiamu, wadzizimbaitsiranji? pakuti ine ndatumidwa kwa iwe ndi mau olasa.