1 Kings 14:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidachotsa ufumu ku banja la Davide ndi kuupereka kwa iwe. Komabe iwe sudafanefane ndi Davide mtumiki wanga, amene ankamvera malamulo anga, ndipo ankanditsata ndi mtima wake wonse, namachita zimene Ine ndimafuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndinalanda nyumba ya Davide ufumu, ndi kuupereka kwa iwe, koma sunafanana ndi Davide mtumiki wanga uja, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ndi mtima wake wonse kuchita zolunjika zokhazokha pamaso panga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinachotsa ufumu ku nyumba ya Davide ndi kuwupereka kwa iwe, koma iwe sunafanane ndi mtumiki wanga Davide, amene ankasunga malamulo anga ndi kunditsata Ine ndi mtima wake wonse, kuchita zolungama zokhazokha pamaso panga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndinalanda nyumba ya Davide ufumu, ndi kuupereka kwa iwe, koma sunafanana ndi Davide mtumiki wanga uja, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ndi mtima wace wonse kucita zolunjika zokha zokha pamaso panga;