1 Kings 14:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwe wachita zoipa kupambana onse amene analipo kale, iwe usanakhale pa mpando waufumu, pakuti wadzipangira milungu ina ndiponso mafano osungunula. Pakutero wandipsetsa mtima kwabasi. Ineyo wanditayiratu kumbuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma wachimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu ina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwe wachita zoyipa kupambana onse amene analipo kale. Wadzipangira milungu ina, mafano a zitsulo. Iweyo wandikwiyitsa ndipo wandiwukira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma wacimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu yina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako;