1 Kings 15:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo adalamulira zaka 41 ku Yerusalemu. Gogo wake wamkazi anali Maaka, mwana wa Abisalomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai mphambu chimodzi, ndipo dzina la amake linali Maaka mwana wa Abisalomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 41. Agogo ake akazi anali Maaka mwana wa Abisalomu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai mphambu cimodzi, ndipo dzina la amace linali Maaka mwana wa Abisalomu.