1 Kings 15:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachotsanso gogo wake Maaka pa udindo wa mfumukazi, chifukwa choti ankapembedza fano lonyansa la Asera. Ndipo Asa adaliphwanya fanolo, nakalitenthera ku khwaŵa la Kidroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamchotsera Maaka amake ulemu wa make wa mfumu, popeza iye anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fano lake, nalitentha ku mtsinje wa Kidroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachotsanso gogo wake Maaka pa udindo wake wa amayi a mfumu, chifukwa choti anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo nakalitentha ku Chigwa cha Kidroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamcotsera Maaka amace ulemu wa mace wa mfumu, popeza iye anapanga fano lonyansitsa likhale cifanizo; ndipo Asa analikha fano lace, nalitentha ku mtsinje wa Kidroni.