1 Kings 15:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Baasayo adapita kukathira nkhondo dziko la Yuda, namangira linga mzinda wa Rama, kuti aziletsa anthu kuloŵa kapena kutuluka m'dziko la Asa, mfumu ya ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Baasa mfumu ya Israele anakwera ndi nkhondo ku Yuda, namanga ku Rama kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Baasa mfumu ya Israeli anapita kukathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo anamangira linga mzinda wa Rama kuletsa kuti wina aliyense asatuluke kapena kulowa mʼdziko la Asa, mfumu ya Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Basa mfumu ya Israyeli anakwera ndi nkhondo ku Yuda, namanga ku Rama kuwaletsa anthu asaturuke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.