1 Kings 15:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Asa adatenga siliva yense pamodzi ndi golide, zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso ku nyumba ya mfumu, napatsira atumiki ake. Ndipo adaŵatuma kuti akazipereke Benihadadi, mwana wa Tabirimoni mdzukulu wa Heziyoni, mfumu ya ku Siriya, amene ankakhala ku Damasiko. Mau a Asa anali akuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golide yense anatsala pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma chili m'nyumba ya Yehova chuma chili m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ake; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Asa anatenga siliva yense pamodzi ndi golide zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso ku nyumba yake yaufumu. Anazipereka kwa atumiki ake, nawatuma kupita nazo kwa Beni-Hadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni, mfumu ya Aramu, amene ankakhala ku Damasiko ndipo anakamuwuza kuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golidi yense anatsala pa cuma ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ciri m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ace; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabrimoni, mwana wa Hezroni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,