1 Kings 15:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tiye tigwirizane ine ndi iwe, monga m'mene ankachitira bambo wanga ndi bambo wako. Ona, ndikukutumizira mphatso za siliva ndi golide. Pita ukaphwanye chigwirizano chako ndi Baasa, mfumu ya ku Israele, kuti sadzandithiranso nkhondo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndatumiza kwa inu mphatso ya siliva ndi golide, tiyeni lilekeke pangano lili pakati pa inu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tiyeni tigwirizane inu ndi ine, monga panali mgwirizano pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Onani, ndikukutumizirani mphatso za siliva ndi golide. Tsopano kathetseni mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti andisiye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndatumiza kwa inu mphatso ya siliva ndi golidi, tiyeni lilekeke pangano liri pakati pa inu ndi Basa mfumu ya Israyeli, kuti andicokere.