1 Kings 15:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu Asa adaitana anthu onse a ku Yuda, osasiya ndi m'modzi yemwe, kuti adzanyamule miyala ndi mitengo, imene Baasa ankamangira linga la Rama. Zimenezi mfumu Asa adamangira linga la Geba m'dziko la Benjamini, ndiponso la Mizipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu Asa anamemeza Ayuda onse, osatsala ndi mmodzi yense; natuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yomwe, akamange nayo Baasa; ndi mfumu Asa anamangira Geba wa ku Benjamini, ndi Mizipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Mfumu Asa analamula anthu onse a ku Yuda osasiya ndi mmodzi yemwe, ndipo anachotsa ku Rama miyala ndi matabwa amene Baasa ankamangira kumeneko. Zipangizo zimenezi Mfumu Asa inamangira linga la Geba ku Benjamini ndi la ku Mizipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu Asa anamemeza Ayuda onse, osatsala ndi mmodzi yense; natuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yomwe, akamange nayo Basa; ndi mfumu Asa anamangira Geba wa ku Benjamini, ndi Mizipa.