1 Kings 15:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito zina za Asa, zamphamvu zake zonse, zinthu zimene adazichita ndi mizinda imene adaimanga, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Koma pa nthaŵi ya ukalamba wake adadwala nthenda ya miyendo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo machitidwe onse ena a Asa, ndi mphamvu yake yonse, ndi zonse anazichita, ndi midzi anaimanga, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Koma masiku a ukalamba wake anadwala mapazi ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ntchito zina za Asa, za mphamvu zake ndi mizinda imene anayimanga ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Koma pa nthawi ya ukalamba wake anadwala nthenda ya mapazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo macitidwe onse ena a Asa, ndi mphamvu yace yonse, ndi zonse anazicita, ndi midzi anaimanga, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda? Koma masiku a ukalamba wace anadwala mapazi ace.