1 Kings 15:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nadabu, mwana wa Yerobowamu, adayamba kulamulira anthu a ku Israele pa chaka chachiŵiri cha ufumu wa Asa wa ku Yuda. Tsono Nadabuyo adalamulira ku Israele zaka ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Nadabu mwana wa Yerobowamu analowa ufumu wa Israele chaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nadabu, mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli mʼchaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Nadabu mwana wa Yerobiamu analowa ufumu wa Israyeli caka caciwiri ca Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.