1 Kings 15:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Baasa mwana wa Ahiya, wa banja la Isakara, adachita chiwembu Nadabuyo. Adamupha ku Gibetoni, mzinda wa Afilisti, pamene Nadabu ndi anthu a ku Israele ankathira nkhondo mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Baasa mwana wa Ahiya, wa nyumba ya Isakara, anampangira chiwembu; ndipo Baasa anamkanthira ku Gibetoni wa Afilisti, popeza Nadabu ndi Aisraele onse adamangira misasa Gibetoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Baasa mwana wa Ahiya, wa banja la Isakara anakonzera Nadabuyo chiwembu, ndipo anamukantha ku Gibetoni, mzinda wa Afilisti, pamene Nadabu ndi anthu onse a ku Israeli anali atawuzungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Basa mwana wa Akiya, wa nyumba ya Isakara, anampangira ciwembu; ndipo Basa anamkanthira ku Gibetoni wa Afilisti, popeza Nadabu ndi Aisrayeli onse adamangira misasa Gibetoni.