1 Kings 15:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atangoloŵa ufumuwo, adapha anthu onse a banja la Yerobowamu. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe wamoyo pa banjapo, mpaka adaonongeratu banja lonselo, malinga ndi mau amene Chauta adaalankhula kudzera mwa mtumiki wake uja Ahiya wa ku Silo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono kunachitika, pokhala mfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobowamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula pa dzanja la mtumiki wake Ahiya wa ku Silo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye atangoyamba kulamulira, anapha anthu onse a banja la Yeroboamu. Sanasiye ndi mmodzi yemwe wamoyo pa banjapo, koma anawononga anthu onse, molingana ndi mawu a Yehova amene anayankhula mwa mtumiki wake Ahiya wa ku Silo
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsonokunacitika, pokhalamfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobiamu, osasiyako wamoyo ndi mmodzi yense wa Yerobiamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula pa dzanja la mtumiki wace Ahiya wa ku Silo;