1 Kings 15:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi zidachitika chifukwa cha machimo a Yerobowamu ndi zimene adachimwitsa nazo anthu a ku Israele, naputa nazo mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa cha machimo a Yerobowamu, amene adachimwa nao, nachimwitsa nao Aisraele, ndi kuutsa kwake kumene anaputa nako mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa cha machimo amene Yeroboamu anachita, ndiponso kuchimwitsa anthu a ku Israeli, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa ca macimo a Yerobiamu, amene adacimwa nao, nacimwitsa nao Aisrayeli, ndi kuutsa kwace kumene anaputa nako mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli.