1 Kings 15:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka chachitatu cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Baasa mwana wa Ahiya adayamba kulamulira anthu a ku Israele ku Tiriza, ndipo adakhala mu ufumu zaka 24.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono Baasa mwana wa Ahiya analowa ufumu wa Israele chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ku Tiriza zaka makumi awiri mphambu zinai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Baasa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Aisraeli onse ku Tiriza, ndipo analamulira zaka 24.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono Basa mwana wa Ahiya analowa ufumu wa Israyeli caka cacitatu ca Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ku Tiriza zaka makomi awiri mphambu zinai.