1 Kings 15:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe chifukwa cha Davideyo, Chauta adapatsa Abiya mwana, kuti azilamulira ku Yerusalemu, iyeyo atafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma chifukwa cha Davideyo Yehova Mulungu wake anampatsa nyali m'Yerusalemu, kumuikira mwana wake pambuyo pake, ndi kukhazikitsa Yerusalemu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe chifukwa cha Davide, Yehova Mulungu wake anamupatsa nyale mu Yerusalemu pomupatsa mwana wolowa mʼmalo mwake ndi kumukhazikitsa kukhala wamphamvu mu Yerusalemu;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma cifukwa ca Davideyo Yehova Mulungu wace anampatsa nyali m'Yerusalemu, kumuikira mwana wace pambuyo pace, ndi kukhazikitsa Yerusalemu;