1 Kings 15:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zidatero chifukwa choti Davide adaachita zolungama pamaso pa Chauta, poti sadapatuke pa zimene Chauta adamlamula masiku onse a moyo wake, kupatula nkhani yokha ija ya Uriya Muhiti uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pakuti Davide anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo sanalephere kusunga chilichonse chimene Yehova anamulamula masiku onse a moyo wake kupatula nkhani ija ya Uriya Mhiti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa kuti Davide adacita colungama pamaso pa Yehova, osapambuka masiku ace onse pa zinthu zonse adamlamulira iye, koma cokhaco cija ca Uriya Mhiti.