1 Kings 16:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimuri adadzaloŵa, napha Elayo. Chinali chaka cha 27 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda. Tsono Zimuriyo adaloŵa ufumu m'malo mwa Ela.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nalowamo Zimiri, namkantha, namupha chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri za Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimuri anadzalowa, namukantha ndi kumupha mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda. Ndipo Zimuriyo anakhala mfumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nalowamo Zimri, namkantha, namupha caka ca makomi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwace.