1 Kings 16:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 27 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Zimuri adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Tiriza, koma adangolamulira masiku asanu ndi aŵiri okha. Nthaŵi imeneyo magulu ankhondo a Aisraele adaali akuzinga mzinda wa Gibetoni. Mzindawo unali wa Afilisti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Asa mfumu ya Yuda, Zimiri anali mfumu masiku asanu ndi awiri ku Tiriza. Ndipo anthu analikumangira misasa Gibetoni wa Afilisti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda, Zimuri analamulira ku Tiriza masiku asanu ndi awiri. Gulu la ankhondo linali litamanga misasa pafupi ndi Gibetoni, mzinda wa Afilisti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Asa mfumu ya Yuda, Zimri anali mfumu masiku asanu ndi awiri ku Tiriza. Ndipo anthu analikumangira misasa Gibetoni wa Afilisti.