1 Kings 16:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe sudaali kanthu konse, ndidachita kukukweza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga a ku Israele. Komabe tsopano wachimwa ngati Yerobowamu, ndipo waŵachimwitsa anthu a ku Israelewo, mwakuti iwo aputa mkwiyo wanga chifukwa cha kuchimwa kwaoko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza ndinakukuza iwe kuchokera kufumbi, ndi kukuika iwe mfumu ya anthu anga Israele, koma iwe unayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi kuchimwitsa anthu anga Israele, kuputa mkwiyo wanga ndi machimo ao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndinakukuza kuchokera pa fumbi ndipo ndinakupanga kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli, koma iwe wakhala ukuyenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchimwitsa anthu anga Aisraeli naputa mkwiyo wanga chifukwa cha machimo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza ndinakukuza iwe kucokera kupfumbi, ndi kukuika iwe mfumu ya anthu anga Israyeli, koma iwe unayenda m'njira ya Yerobiamu, ndi kucimwitsa anthu anga Israyeli, kuputa mkwiyo wanga ndi macimo ao;