1 Kings 16:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu otsata Omuri adagonjetsa anthu otsata Tibini, mwana wa Ginati. Choncho Tibini adafa, ndipo Omuri adaloŵa ufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anthu akutsata Omuri anapambana iwo akutsata Tibini mwana wa Ginati; nafa Tibini, Omuri nakhala mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu otsatira Omuri anali amphamvu kupambana amene ankatsatira Tibini mwana wa Ginati. Choncho Tibini anafa ndipo Omuri anakhala mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anthu akutsata Omri anapambana iwo akutsata Tibini mwana wa Ginati; nafa Tibini, Omri nakhala mfumu.