1 Kings 16:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adagula phiri la Samariya kwa Semeri pa mtengo wa ndalama 6,000 zasiliva. Ndipo adamangapo mzinda, namanganso linga kutchinjiriza phirilo. Mzinda umene adaumangawo adautcha Samariya, potsata dzina la Semeri, mwini wake wa phirilo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anagula kwa Semeri chitunda cha Samariya ndi matalente awiri a siliva, namanga pachitundapo, natcha dzina lake la mudzi anaumanga Samariya, monga mwa dzina la Semeri mwini chitundacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anagula phiri la Samariya kwa Semeri pa mtengo wa ndalama 6,000 za siliva ndipo pa phiripo anamangapo mzinda, nawutcha Samariya, potsata dzina la Semeri, dzina la mwini wakale wa phirilo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anagula kwa Semeri citunda ca Samaria ndi matalente awiri a siliva, namanga pacitundapo, nacha dzina lace la mudzi anaumanga Samaria, monga mwa dzina la Semeri mwini citundaco.