1 Kings 16:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankachita zoipa ngati Yerobowamu, mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo anthu a ku Israele, naputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, popembedza mafano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nayenda m'njira yonse ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi tchimo lake anachimwitsa nalo Aisraele, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele ndi zachabe zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti iye anayenda mʼnjira zonse za Yeroboamu mwana wa Nebati, ndipo tchimo lake anachimwitsa nalo Aisraeli, nakwiyitsa Yehova Mulungu wa Israeli ndi mafano awo opandapake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nayenda m'njira yonse ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi chimo lace anacimwitsa nalo Aisrayeli, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli ndi zacabe zao.