1 Kings 16:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 38 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Ahabu mwana wa Omuri, adaloŵa ufumu wa ku Israele. Iyeyo adalamulira anthu a ku Israele ku Samariya zaka 22.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Asa mfumu ya Yuda Ahabu mwana wa Omuri analowa ufumu wa Israele, nakhala Ahabu mwana wa Omuri mfumu ya Israele m'Samariya zaka makumi awiri mphambu ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 38 cha ufumu wa Asa, mfumu ya Yuda, Ahabu mwana wa Omuri anakhala mfumu ya Israeli nalamulira Israeli ku Samariya zaka 22.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu ca Asa mfumu ya Yuda Ahabu mwana wa Omri analowa ufumu wa Israyeli, nakhala Ahabu mwana wa Omri mfumu ya Israyeli m'Samaria zaka makumi awiri mphambu ziwiri.