1 Kings 16:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachita ngati sadakhutire ndi kuchimwa konga kwa Yerobowamu, mwakuti adaonjeza tchimo pakukwatira Yezebele, mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni, nayamba kutumikira fano lotchedwa Baala, ndi kumalipembedza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m'machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikira Baala, namgwadira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sanachiyese ngati chinthu chochepa chabe kuchita machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, koma anakwatiranso Yezebeli, mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni, nayamba kutumikira Baala ndi kumupembedza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali monga ngati kunamcepera kuyenda m'macimo a Yerobiamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebeli mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Azidoni, natumikira Baala, namgwadira,