1 Kings 16:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo m'nyumbamo adamangamo guwa la Baalayo, naimikamo fano la Asera. Motero Ahabu adachita zinthu zambiri zoputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, kupambana mafumu onse a ku Israele amene adaalipo kale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ahabu anapanganso chifanizo; ndipo Ahabu amene anapambana mafumu onse a Israele adamtsogolerawo, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahabu anapanganso fano la Asera ndi kukwiyitsa kwambiri Yehova Mulungu wa Israeli, kupambana mafumu onse a Israeli amene analipo iye asanakhale mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ahabu anapanganso cifanizo; ndipo Ahabu amene anapambana mafumu onse a Israyeli adamtsogolerawo, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli,