1 Kings 16:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku a mfumu Ahabu, Hiyele wa ku Betele adamanganso mzinda wa Yeriko. Koma monga adaaneneratu Chauta kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni, Abiramu, mwana wamwamuna wachisamba wa Hiyele, adamwalira pa nthaŵi yomanga maziko a mzindawo. Kenaka Segubu, mzime wake, nayenso adamwalira pa nthaŵi yomanga zipata za mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'masiku ake Hiyele wa ku Betele anamanga Yeriko; pokhazika maziko ake anadzifetsera Abiramu mwana wake woyamba, poimika zitseko zake anadzifetsera Segubu mwana wake wotsiriza; monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi ya Ahabu, Hiyeli wa ku Beteli anamanganso mzinda wa Yeriko. Pa nthawi yomanga maziko ake, mwana wake woyamba wa mwamuna, Abiramu anamwalira, ndipo pa nthawi yomanga zipata zake, mwana wa mngʼono wa mwamuna Segubu, anamwaliranso. Izi zinachitika monga momwe Yehova ananenera kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'masiku ace Hiyeli wa ku Beteli anamanga Yeriko; pokhazika maziko ace anadzifetsera Abiramu mwana wace woyamba, poimika zitseko zace anadzifetsera Zegubi mwana wace wotsiriza; monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni.