1 Kings 16:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asanafe Baasa, Chauta adalankhula kudzera mwa mneneri Yehu, mwana wa Hanani, mau omuzenga mlandu Baasa pamodzi ndi banja lake lonse, chifukwa cha zoipa zonse zimene adaachita pamaso pa Chauta. Iyeyo adaputa mkwiyo wa Chauta ndi machimo amene ankachita, olingana ndi a anthu a banja la Yerobowamu, ndiponso chifukwa choti adaaonongeratu banja lonse la Yerobowamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Baasa ndi nyumba yake, chifukwa cha zoipa zonse anazichita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wake ndi machitidwe a manja ake, nafanana ndi nyumba ya Yerobowamu; ndiponso popeza anaikantha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu Yehova anayankhula kwa Baasa pamodzi ndi banja lake lonse kudzera mwa mneneri Yehu mwana wa Hanani, chifukwa cha zoyipa zonse zimene iye anachita pamaso pa Yehova, kukwiyitsa Yehovayo nakhala ngati nyumba ya Yeroboamu ndiponso chifukwa anawonongeratu banja la Yeroboamu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Basa ndi nyumba yace, cifukwa ca zoipa zonse anazicita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wace ndi macitidwe a manja ace, nafanana ndi nyumba ya Yerobiamu; ndiponso popeza anaikantha.