1 Kings 16:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono munthu wina dzina lake Zimuri, amene anali mkulu woyang'anira hafu la magaleta ake, adamchita chiwembu. Pamene Elayo anali ku Tiriza, namamwa mpaka kuledzera m'nyumba ya Ariza, amene ankayang'anira nyumba yachifumu ku Tirizako,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mnyamata wake Zimiri, ndiye woyang'anira dera lina la magaleta ake, anampangira chiwembu; koma iye anali m'Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba m'Tiriza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimuri, mmodzi mwa akuluakulu ake, amene ankalamulira theka la magaleta ake, anamuchitira chiwembu. Nthawi imeneyi Ela anali ku Tiriza, akumwa koledzera nako mʼnyumba ya Ariza, munthu amene ankayangʼanira nyumba yaufumu ku Tiriza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mnyamata wace Zimri, ndiye woyang'anira dera lina la magareta ace, anampangira ciwembu; koma iye anali m'Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba m'Tiriza.