1 Kings 17:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, adauza Ahabu kuti, “Pali Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene ndimamtumikira, sipakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, mpaka ine ntanena.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, anati kwa Ahabu, “Pali Yehova wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene ndimamutumikira, sipadzakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditanena.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Gileadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israyeli, amene ndimakhala pamaso pace, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.