1 Kings 17:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Eliya adanyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, adangoona mai wamasiye akutola nkhuni. Tsono adaitana maiyo namuuza kuti, “Patseniko madzi pang'ono, ndimwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono iye ananyamuka namka ku Zarefati, nafika ku chipata cha mudzi; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'chikho, ndimwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho iye ananyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, taonani mkazi wamasiye amatola nkhuni. Anamuyitana ndi kumuwuza kuti, “Patseni madzi pangʼono mʼchikho kuti ndimwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono iye ananyamuka namka ku Zarefati, nafika ku cipata ca mudzi; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'cikho, ndimwe.