1 Kings 17:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo maiyo adati, “Pali Chauta, Mulungu wanu, ine sindidaphike kanthu kalikonse, koma ndili ndi ufa pang'ono m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa. Tsono ndikutola nkhuni zoti ndikaphikire kaufako, kuti ndikadye ine ndi mwana wanga, kenaka kufa kukhala komweko.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndilibe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndilikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire ndekha ndi mwana wanga, tidye, tife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ine ndilibe chakudya china chilichonse, koma kaufa pangʼono mʼmbiya ndi mafuta pangʼono mʼbotolo. Ine ndikutola tinkhuni tochepa kuti ndipite nato ku nyumba ndi kukaphika chakudya changa ndi cha mwana wanga, kuti tikadye kenaka tife.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndiribe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndirikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire odekha ndi mwana wanga, tidye, tife.