1 Kings 17:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Ufa umene uli m'mbiyawo sudzatha, mafutanso amene ali m'nsupawo sadzatha, mpaka tsiku limene Chauta adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzachepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ufa umene uli mʼmbiyamo sudzatha ndipo mafuta amene ali mʼbotolomo sadzathanso mpaka tsiku limene Yehova adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzacepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova pa dziko lapansi.