1 Kings 17:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono maiyo adapita, nakachitadi monga momwe adaanenera Eliya. Maiyo ndi Eliya ndiponso onse a pa banja la maiyo adadya ufawo masiku ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anakachita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m'nyumba ake, masiku ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayi wamasiyeyo anapita nakachita zimene Eliya anamuwuza. Choncho panali chakudya cha Eliya, mayiyo pamodzi ndi banja lake lonse chimene anadya masiku ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anakacita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m'nyumba ace, masiku ambiri.