1 Kings 17:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi uja adafunsa Eliya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu mneneri wa Mulungu? Kodi mwadza kwa ine kuno kudzakumbutsa Mulungu machimo anga ndi kundiphera mwana wanga?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayiyo anati kwa Eliya, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu munthu wa Mulungu? Kodi munabwera kuno kudzandikumbutsa tchimo langa ndi kudzandiphera mwana wanga?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndiri nawe ciani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa chimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?