1 Kings 17:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Eliya adauza maiyo kuti, “Tandipatsani mwanayo.” Pompo Eliya adatenga mwanayo pa mfukato ya mai uja, napita naye ku chipinda chapamwamba, kumene ankagona, ndipo adakamgoneka pa bedi lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m'mfukato mwake napita naye ku chipinda chosanja chogonamo iyeyo, namgoneka pa kama wa iye mwini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya anayankha kuti, “Patseni mwana wanuyo.” Iye anatenga mwanayo mʼmanja mwa mayiyo napita naye mʼchipinda chapamwamba, kumene Eliyayo amagona, namugoneka pa bedi lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m'mfukato mwace napita naye ku cipinda cosanja cogonamo iyeyo; namgoneka pa kama wa iye mwini.