1 Kings 18:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pali Chauta, Mulungu wanu wamoyo, kulibe mtundu wa anthu kapena ufumu uliwonse kumene mbuyanga Ahabu sadatumeko anthu okakufunafunani. Anthu akamuuza kuti, ‘Eliya kulibe kuno,’ Ahabu ankaŵalumbiritsa anthuwo kuti atsimikizedi ngati inu kunalibe kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sananditumeko kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezeni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, kulibe mtundu wa anthu kapena ufumu uliwonse kumene mbuye wanga sanatumeko anthu okakufunafunani. Ndipo pamene mtundu wa anthu kapena ufumu unena kuti kuno kulibe, Ahabu ankawalumbiritsa kuti atsimikizedi kuti inuyo kulibe kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sanatumako kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezani.