1 Kings 18:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi inu mbuyanga simudamve zoti nthaŵi imene Yezebele ankapha aneneri a Chauta, ine ndidabisa aneneri 100 a Chauta, anthu 50 m'phanga limodzi, 50 ena m'phanga lina, ndipo kuti ndinkaŵadyetsa chakudya ndi kumaŵapatsa madzi akumwa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m'kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanuasanu m'phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbuye wanga, kodi simunamve zimene ndinachita pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova? Ine ndinabisa aneneri 100 a Yehova mʼmapanga awiri, mʼphanga lililonse aneneri makumi asanu, ndipo ndinkawapatsa chakudya ndi madzi akumwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi sanakuuzani mbuye wanga cimene ndidacita m'kuwapha Yezebeli aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndikuwadyetsa mkate ndi madzi?